Marko 11:29-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani mau amodzi, mundiyankhe Ine, ndipo ndidzakuuzani ulamuliro umene ndicita nao zinthu zimenezi.

30. Ubatizo wa Yohane ucokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu? Mundiyankhe.

31. Ndipo anatsutsana mwa iwo okha, nanena, Tikati, Kumwamba; adzanena iye, Ndipo simunakhulupirira iye bwanji?

Marko 11