47. Ndipo pamene anamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, anayamba kupfuula, ndi kunena, Yesu, Inu Mwana wa Davide, mundicitire ine cifundo.
48. Ndipo ambiri anamuyamula kuti atonthole: koma makamaka anapfuulitsa kuti, Inu Mwana wa Davide, mundicitire cifundo.
49. Ndipo Yesu anaima, nati, Mwitaneni. Ndipo anaitana wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka, akuitana.
50. Ndipo iye anataya copfunda cace, nazunzuka, nadza kwa Yesu.
51. Ndipo Yesu anamyankha, nati, Ufuna kuti ndikucitire ciani? Ndipo wakhunguyo anati kwa Iye, Raboni, ndilandire kuona kwanga.