1. CIYAMBI cace ca Uthenga Wabwino wa Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu.
2. Monga mwalembedwa m'Yesaya mneneri,Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu,Amene adzakonza njira yanu;
3. Mau a wopfuula m'cipululu, Konzani khwalala la Ambuye, Lungamitsani njira zace;
4. Yohane anadza nabatiza m'cipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku cikhululukiro ca macimo.
5. Ndipo anaturuka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordano, poulula macimo ao.
6. Ndipo Yohane anabvala ubweya wa ngamila, ndi lamba lacikopa m'cuuno mwace, nadya dzombe ndi uci wa kuthengo.