Maliro 4:8-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Maonekedwe ao ada koposa makala, sazindikirika m'makwalala;Khungu lao limamatira pa mafupa ao, lakhwinyata, lasanduka ngati ndodo.

9. Ophedwa ndi lupanga amva bwino kupambana ophedwa ndi njala;Pakuti amenewa angokwalika napyozedwa, posowa zipatso za m'munda.

10. Manja a akazi acisoni anaphika anaanao;Anali cakudya cao poonongeka mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.

11. Yehova wakwaniritsa kuzaza kwace, watsanulira ukali wace;Anayatsa moto m'Ziyoni, unanyambita maziko ace,

12. Mafumu a dziko lapansi sanakhulupirira, ngakhale onse okhala kunja kuno,Kuti adani ndi amaliwongo adzalowadi m'zipata za Yerusalemu.

13. Ndico cifukwa ca macimo a aneneri ndi mphulupulu za ansembeace,Amene anakhetsa mwazi wa olungama pakati pace.

14. Asocera m'makwalala ngati akhungu, aipsidwa ndi mwazi;Anthu sangakhudze zobvala zao.

15. Amapfuula kwa iwo, Cokani, osakonzeka inu, cokani, cokani, musakhudze kanthu.Pothawa iwo ndi kusocera, anthu anati mwa amitundu, Sadzagoneranso kuno.

16. Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso;Iwo sanalemekeza ansembe, sanakomera mtima akulu.

Maliro 4