7. Omveka ace anakonzeka koposa cipale cofewa, nayera koposa mkaka,Matupi ao anafiira koposa timiyala toti pyu; maonekedwe ao ananga a safiro wa mtengo wapatari.
8. Maonekedwe ao ada koposa makala, sazindikirika m'makwalala;Khungu lao limamatira pa mafupa ao, lakhwinyata, lasanduka ngati ndodo.
9. Ophedwa ndi lupanga amva bwino kupambana ophedwa ndi njala;Pakuti amenewa angokwalika napyozedwa, posowa zipatso za m'munda.
10. Manja a akazi acisoni anaphika anaanao;Anali cakudya cao poonongeka mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.