61. Mwamva citonzo cao, Yehova, ndi zopangira zao zonse za pa ine,
62. Milomo ya akutsutsana nane ndi zolingalira zao za pa ine tsiku lonse.
63. Taonani kukhala ndi kunyamuka kwao; ndine nyimbo yao.
64. Mudzawabwezera cilango, Yehova, monga mwa macitidwe a manja ao;
65. Muphimbe mtima wao ndi kuwatemberera;
66. Mudzawalondola mokwiya ndi kuwaononga pansi pa thambo la Yehova.