Maliro 3:24-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Moyo wanga uti, Gawo langa ndiye Yehova; cifukwa cace ndidzakhulupirira.

25. Yehova akhalira wabwino omlindirira, ndi moyo womfunafuna.

26. Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha cipulumutso ca Yehova.

27. Nkokoma kuti munthu asenze gori ali wamng'ono.

Maliro 3