1. Ine ndine munthuyu wakuona msauko ndi ndodo ya ukali wace.
2. Wanditsogolera, nandiyendetsa mumdima, si m'kuunika ai.
3. Zoonadi amandibwezera-bwezera dzanja lace monditsutsa tsiku lonse.
4. Wagugitsa thupi langa ndi khungu langa, natyola mafupa anga.