Maliro 1:4-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. M'njira za Ziyoni mulira posoweka akudzera msonkhano;Pa zipata zace zonse papasuka; ansembe ace onse ausa moyo;Anamwali ace asautsidwa; iye mwini namva zowawa.

5. Amaliwongo ace asanduka akuru ace, adani ace napindula;Pakuti Yehova wamsautsa pocuruka zolakwa zace;Ana ace ang'ono alowa m'ndende pamaso pa adani ace.

6. Ulemu wace wonse wamcokera mwana wamkazi wa Ziyoni;Akalonga ace asanduka nswala zosapeza busa,Anayenda opanda mphamvu pamaso pa wompitikitsa.

7. M'masiku a msauko wace ndi kusocera kwaceYerusalemu ukumbukira zokondweretsa zace zonse zacikhalire;Pogwidwa anthu ace ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa,Adaniwo anamuona naseka mwacipongwe mabwinja ace.

8. Yerusalemu wacimwa kwambiri; cifukwa cace wasanduka cinthu conyansa;Onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamarisece;Inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo.

9. Udio wace unali m'nsaru zace; sunakumbukira citsiriziro cace;Cifukwa cace watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza;Taonani Yehova, msauko wanga, pakuti mdaniyo wadzikuzayekha.

Maliro 1