Malaki 3:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kacisi wace modzidzimutsa; ndiye mthenga wa cipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.

2. Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwace? ndipo adzaima ndani pooneka Iye? pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka;

3. ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golidi ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m'cilungamo.

4. Pamenepo copereka ca Yuda ndi Yerusalemu cidzakomera Yehova, ngati masiku a kale lija ndi ngati zaka zoyamba zija.

5. Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi acigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa nchito pa kulipira kwace, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.

Malaki 3