4. Cinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawacha, Dziko la coipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao cikwiyire.
5. Ndipo maso anu adzaona, nimudzati, Yehova ali wamkuru kupitirira malire a Israyeli.
6. Mwana alemekeza atate wace, ndi mnyamata mbuye wace; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?
7. Mupereka mkate wodetsedwa pa guwa langa la nsembe; ndipo mukuti, Takudetsani motani? M'menemo, mwakuti munena, Gome la Yehova nlonyozeka.