Macitidwe 9:22-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Koma Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala m'Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Kristu.

23. Ndipo atapita masiku ambiri, Ayuda anapangana kuti amuphe iye;

24. koma ciwembu cao cinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe;

25. koma ophunzira ace anamtenga usiku, nampyoletsa palinga, namtsitsa ndi mtanga,

26. Koma m'mene anafika ku Yerusalemu, anayesa kudziphatika kwa ophunzira; ndipo anamuopa iye onse, osakhulupirira kuti ali wophunzira.

27. Koma Bamaba anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti m'Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu.

28. Ndipo anali pamodzi nao, nalowa naturuka ku Yerusalemu,

Macitidwe 9