27. Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mudzi muno Herode, ndi Pontiyo Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israyeli kumcitira coipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;
28. kuti acite ziri zonse dzanja lanu ndi uphungu wanu zidaweruziratu zicitike.
29. Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse,
30. m'mene mutambasula dzanja lanu kukaciritsa; ndi kuti zizindikilo ndi zozizwa zicitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.