Macitidwe 3:24-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Koma angakhale aneneri onse kuyambira Samuelindi akumtsatira, onse amene analankhula analalikira za masiku awa.

25. Inu ndinu ana a aneneri, ndi a panganolo Mulungu anapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbeu yako mafuko onse a dziko adzadalitsidwa.

26. Kuyambira ndi inu, Mulungu, ataukitsa Mwana wace, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwezani yense ku zoipa zace.

Macitidwe 3