8. Ndipo kunatero kuti atate wace wa Popliyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, namciritsa.
9. Ndipo patacitika ici, enanso a m'cisumbu, okhala nazo nthenda, anadza, naciritsidwa;
10. amenenso anaticitira ulemu wambiri; ndipo pocoka ife anatiikira zotisowa.
11. Ndipo itapita miyezi itatu tinayenda m'ngalawa ya ku Alesandriya, idagonera nyengo ya cisanu kucisumbuko, cizindikilo cace, Ana-a-mapasa.
12. Ndipo pamene tinakoceza ku Surakusa, tinatsotsako masiku atatu.
13. Ndipo pocokapo tinapaza ntifika ku Regio; ndipo litapita tsiku limodzi unayamba mwela, ndipo m'mawa mwace tinafika ku Potiyolo:
14. pamenepo tinakomana ndi abale, amene anatiumirira tikhale nao masiku asanu ndi awiri; ndipo potero tinafika ku Roma.
15. Kucokera kumeneko abalewo, pakumva za ife, anadza kukomana nafe ku Bwalo la Apiyo, ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu; ndipo pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima.
16. Ndipo pamene tinalowa m'Roma, analola Paulo akhale pa yekha ndi msilikari womdikira iye.