Macitidwe 28:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo titapulumuka, pamenepo tinadziwa kuti cisumbuco cinachedwa Melita.

2. Ndipo akunja anaticitira zokoma zosacitika pena ponsepo; pakuti anasonkha moto, natilandira ife tonse, cifukwa ca mvula inalinkugwa, ndi cifukwa ca cisanu.

3. Koma pamene Paulo adaola cisakata ca nkhuni, naciika pamoto, inaturukamo njoka, cifukwa ca kutenthaku, nilumadzanja lace.

Macitidwe 28