Macitidwe 27:42-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

42. Ndipo uphungu wa asilikari udati awapheandende, angasambire, ndi kuthawa.

43. Koma kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, anawaletsa angacite ca uphungu wao; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziporiya m'nyanja, nafike pamtunda,

44. ndipo otsalawo, ena pamatabwa, ndi ena pa zina za m'ngalawa. Ndipo kudatero kuti lonse adapulumukira pamtunda.

Macitidwe 27