8. Muciyesa cinthu cosakhulupirika, cakuti Mulungu aukitsa akufa?
9. Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kucita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.
10. Cimenenso ndinacita m'Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe akulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinabvomerezapo.
11. Ndipo ndinawalanga kawiri kawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukuru pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira ku midzi yakunja.
12. M'menemo popita ine ku Damasiko ndi ulamuliro ndi ukumu wa kwa ansembe akulu, dzuwa lamsana,