Macitidwe 23:7-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo pamene adatero, kunakhala cilekano pakati pa Afarisi ndi Asaduki; ndipo osonkhanawo anagawikana.

8. Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuuka kwa akufa, kapena mngelo, kapena mzimu; koma Afarisi abvomereza ponse pawiri.

9. Ndipo cidauka cipolowe cacikuru; ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza coipa ciri conse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo: walankhula naye?

10. Ndipo pamene padauka cipolowe cacikuru, kapitao wamkuru anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikari atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga,

11. Ndipo usiku wace Ambuye anaimirira pa iye, nati, Limbika mtima; pakuti monga wandicitira umboni ku Yerusalemu, koteronso uyenera kundicitira umboni ku Roma.

12. Ndipo kutaca, Ayuda anapangana ciwembu, nadzitemberera, ndi kunena kuti sadzadya kapena kumwa kanthu, kufikira atamupha Paulo;

13. ndipo iwo amene adacita cilumbiro ici anali oposa makumi anai.

14. Amenewo anadza kwa ansembe akulu ndi akulu, nati, Tadzitemberera nalo temberero kuti sitidzalawa kanthu kufikira titamupha Paulo.

15. Potero tsopano inu ndi bwalo la akuru muzindikiritse kapitao wamkuru kuti atsikenaye kwa inu, monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asanayandikire iye.

Macitidwe 23