Macitidwe 22:11-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo popeza sindinapenya, cifukwa ca ulemerero wa kuunikako, anandigwira dzanja iwo amene anali ndi ine, ndipo ndinafika ku Damasiko.

12. Ndipo munthu dzina lace Hananiya, ndiye munthu wopembedza monga mwa cilamulo, amene amcitira umboni wabwino Ayuda onse akukhalako,

13. anadza kwa ine, ndipo poimirirapo anati kwa ine, Saulo, mbale, penyanso. Ndipo ine, ora lomweli ndinampenya.

Macitidwe 22