Macitidwe 22:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Amuna, abale, ndi atate, mverani codzikanira canga tsopano, ca kwa inu.

2. Ndipo pakumva kuti analankhula nao m'cinenedwe ca Cihebri, anaposa kukhala cete; ndipo anati:

3. ine ndine munthu Myuda, wobadwa m'Tariso wa Kilikiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliyeli, wolangizidwa monga mwa citsatidwe ceni ceni ca cilamulo ca makolo athu, ndipo ndinali wacangu, colinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;

4. ndipo ndinalondalonda Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi.

Macitidwe 22