Macitidwe 2:21-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina laAmbuye adzapulumutsidwa.

22. Amuna inu Aisrayeli, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wocokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndizimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikilo, zimene Mulungu anazicita mwa iye pakati pa inu, monga mudziwa nokha;

23. ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampacika ndi kumupha ndi manja a anthu osayeruzika;

24. yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti iye agwidwe nayo.

Macitidwe 2