30. nawaturutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndicitenji kuti ndipulumuke?
31. Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.
32. Ndipo anamuuza iye mau a Ambuye, pamodzi ndi onse a pabanja pace.
33. Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pace.
34. Ndipo anakwera nao kunka kunyumba kwace, nawakhazikira cakudya, nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pace, atakhulupirira Mulungu.
35. Kutaca, oweruza anatumiza akapitao, kuti, Mukamasule anthu aja.