Macitidwe 13:38-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Potero padziwike ndi inu amuna abale, 5 kuti mwa iye cilalikidwa kwa inu cikhululukiro ca macimo;

39. ndipo 6 mwa iye yense wokhulupira ayesedwa wolungama kumcotsera zonse zimene simunangathe kudzicotsera poyesedwa wolungama ndi cilamulo ca Mose.

40. Cifukwa cace penyerani, kuti cingadzere inu conenedwa ndi anenenwo:

41. 7 Taona ni, opeputsa inu, zizwani, kanganukani;Kuti ndigwiritsa nchito Ine masikuanu,Nchito imene simudzaikhulupira wina akakuuzani.

42. Ndipo pakuturuka iwo anapempha kuti alankhule naonso mau awa Sabata likudzalo.

43. Ndipo m'mene anthu a m'sunagoge anabalalika, Ayuda ambiri ndi akupinduka opembedza anatsata. Paulo ndi Bamaba; amene, polankhula nao, 8 anawaumiriza akhale m'cisomo ca Ambuye.

44. Ndipo Sabata linalo udasonkhana pamodzi ngati mudzi wonse kumva mau a Mulungu.

45. Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nacita mwano.

46. Ndipo Paulo ndi Bamaba analimbika mtima ponena, nati, 9 Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. 10 Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu.

Macitidwe 13