Macitidwe 1:8-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ace a dziko.

9. Ndipo m'mene adanena izi, ali cipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira iye kumcotsa kumaso kwao.

10. Ndipo pakukhala iwo cipenyerere kumwamba pomuka iye, taonani, amuna awiri obvala zoyera anaimirira pambali pao;

Macitidwe 1