Luka 9:2-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo anawatuma kukalalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuciritsa anthu odwala.

3. Ndipo iye anati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndarama; ndipo musakhale nao malaya awiri.

4. Ndipo m'nyumba iri yonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikacokera kumeneko.

5. Ndipo onse amene sakakulandireni inu, m'mene muturuka m'mudzi womwewo, sansani pfumbi la pa mapazi anu, likhale mboni ya paiwo.

Luka 9