Luka 4:42-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

42. Ndipo kutaca anaturuka iye nanka ku malo acipululu; ndi makamu a anthu analikwnfunafuna iye, nadza nafika kwa iye, nayesa kumletsa iye, kuti asawacokere.

43. Koma anati kwa iwo, Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku midzi yinanso: cifukwa ndinatumidwa kudzatero.

44. Ndipo iye analikulalikira m'masunagoge a ku Galileya.

Luka 4