Luka 24:39-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

39. Penyani manja anga ndi mapazianga, kuti Ine ndine mwini: 2 ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe, mnofu ndi mafupa, monga muona ndirinazo Ine.

40. Ndipo m'mene ananena ici, anawaonetsera iwo manja ace ndi mapazi ace.

41. Koma pokhala iwo cikhalire osakhulupirira cifukwa ca cimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, 3 Muli nako kanthu kakudya kuno?

42. Ndipo anampatsa iye cidutsu ca nsomba yokazinga.

43. Ndipo 4 anacitenga, nacidya pamaso pao.

Luka 24