45. Ndipo nsaru yocinga ya m'Kacisi inang'ambika pakati.
46. Ndipo pamene Yesu anapfuula ndi mau akuru, anati, 1 Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wace.
47. Ndipo 2 pamene kenturiyo anaona cinacitikaco, analemekeza Mulungu, nanena, Zoonadi munthu uyu anali wolungama.
48. Ndipo makamu onse osonkhana kudzapenya ici, pamene anaona zinacitikazo, anapita kwao ndi kudziguguda pacifuwa.