7. Ndipo iye anabala mwana wace wamwamuna woyamba; namkulunga iye m'nsaru, namgoneka modyera ng'ombe, cifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.
8. Ndipo panali abusa m'dziko lomwelo, okhala kubusa ndi kuyang'anira zoweta zao usiku.
9. Ndipo mngelo wa Ambuye anaimirira pa awo, ndi kuwala kwa Ambuye kunawaunikira kozungulira: ndipo anaopa ndi mantha akuru.
10. Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa cikondwero cacikuru, cimene cidzakhala kwa anthu onse;