Luka 19:46-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

46. Kwalembedwa, Ndipo nyumba yanga idzakhala nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa iyo phanga la acifwamba.

47. Ndipo analikuphunzitsa m'Kacisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe akulu, ndi alembi ndi akulu a anthu anafunafuna kumuononga iye;

48. ndipo sanapeza cimene akacita; pakuti anthu onse anamlendewera iye kuti amve.

Luka 19