Luka 14:28-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, nawerengera mtengo wace, aone ngati ali nazo zakuimariza?

29. Kuti kungacitike, pamene atakhazika pansi miyala ya ku maziko ace, osakhoza kuimariza, anthu onse akuyang'ana adzayamba kumseka iye,

30. ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumariza.

Luka 14