Luka 1:77-80 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

77. Kuwapatsa anthu ace adziwitse cipulumutso,21 Ndi makhululukidwe a macimoao,

78. Cifukwa ca mtima wacifundo wa Mulungu wathu.M'menemo mbanda kuca wa kumwamba udzaticezera ife;

79. 22 Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa;Kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.

80. Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wace, ndipo 23 iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israyeli.

Luka 1