Levitiko 7:15-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Kunena za nyama ya nsembe volemekeza ya nsembe zoyamika zace, aziidya tsiku lomwelo lakuipereka; asasiyeko kufikira m'mawa.

16. Koma nsembe ya copereka cace ikakhala ya cowinda, kapena copereka caufuhi, aidye tsiku lomwelo anabwera nayo nsembe yace; ndipo m'mawa adye cotsalirapo;

17. koma cotsalira pa nyama ya nsembeyo tsiku lacitatu, acitenthe.

18. Ndipo akadyako nyama ya nsembe zoyamika zace tsiku lacitatu, sikubvomerezeka kumene; sadzamwerengera wobwera nayo; ndiyo cinthu conyansa, ndipo munthu wakudyako adzasenza mphulupulu zace.

19. Ndipo nyama yokhudza kanthu kali konse kodetsa isadyeke; aitenthe ndi moto. Koma za nyama yina, ali yense ayera aidyeko.

20. Koma munthu akadya nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, pokhala naco comdetsa, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.

Levitiko 7