Levitiko 24:6-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo utiike m'mizere iwiri, tisanu ndi kamodzi mzere umodzi, pa gome loyera, pamaso pa Yehova.

7. Nuike libano loona ku mzere uli wonse, kuti likhale kumkate ngati cokumbutsa, nsembe yamoto ya Yehova.

8. Nthawi zonse tsiku la Sabata aukonze pamaso pa Yehova, cifukwa ca ana a Israyeli, ndilo pangano losatha.

9. Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ace, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulikitsa wocokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha.

10. Ndipo mwana wamwamuna wa mkazi M-israyeli, atate wace ndiye M-aigupto, anaturuka mwa ana a Israyeli; ndi mwana wamwamuna wa mkazi M-israyeliyo analimbana naye munthu M-israyeli kucigono;

11. ndipo mwana wamwamuna wa mkazi M-israyeli anacitira DZINA mwano, natemberera; ndipo anadza naye kwa Mose. Dzina la mai wace ndiye Selomiti, mwana wa Dibri, wa pfuko la Dani.

Levitiko 24