3. ndi cifukwa ca mlongo wace weni weni, akakhala namwali wosakhala naye mwamuna, nkuloleka adzidetse cifukwa ca iwowa.
4. Akakhala mwini banja pakati pa anthu a mtundu wace, asadzidetse, ndi kudziipsa,
5. Asamete tsitsi la pamtu pao, kapena kucecerera ndebvu zao, kapena kudziceka matupi ao.
6. Azikhala opatulikira Mulungu wao, osaipsa dzina la Mulungu wao; popeza amapereka nsembe zamoto za Yehova, mkate wa Mulungu wao; cifukwa cace akhale opatulika.
7. Asadzitengere mkazi wacigololo, kapena woipsidwa; asatenge mkazi woti adamcotsa mwamuna wace; popeza apatulikira Mulungu wace.