22. Adye cakudya ca Mulungu wace, copatulikitsa, ndi copatulika;
23. koma asafike ku nsaru yocinga, asayandikize ku guwa la nsembe, popeza ali naco cirema; kuti angaipse malo anga opatulika; popeza Ine ndine Yehova wakuwapatula.
24. Momwemo Mose ananena ndi Aroni, ndi ana ace amuna, ndi ana onse a Israyeli.