Levitiko 21:10-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo iye wokhala mkulu wansembe mwa abale ace, amene anamtsanulira mafuta odzoza pamutu pace, amene anamdzaza dzanja kuti abvale zobvalazo, asawinde, kapena kung'amba zobvala zace.

11. Asafike kuli mtembo; asadzidetse cifukwa ca atate wace, kapena mai wace.

12. Asaturuke m'malo opatulika, kapena kuipsa malo opatulika a Mulungu wace; popeza korona wa mafuta odzoza wa Mulungu wace ali pa iye; Ine ndine Yehova.

13. Ndipo adzitengere mkazi akali namwali.

14. Mkazi wamasiye, kapena womleka, kapena woipsidwa, wacigololo, oterewa asawatenge; koma azitenga namwali wa anthu a mtundu wace akhale mkazi wace.

Levitiko 21