14. Usamatemberera wogontha; usamaika cokhumudwitsa pamaso pa wosaona; koma uziopa Mulungu wako; Ine ndine Yehova.
15. Musamacita cisalungamo pakuwemza mlandu; usamabvomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.
16. Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.
17. Usamamuda mbale wako mumtima mwako; umdzudzule munthu mnzako ndithu, usadzitengera ucimo cifukwa ca iye.
18. Usamabwezera cilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha; Ine ndine Yehova.
19. Muzisunga malemba anga, Usamalola zoweta zako za mitundu yosiyana zikwerane; usamabzala m'munda mwako mbeu za mitundu iwiri; usamabvala cobvala ca nsaru za mitundu iwiri zosokonezana.