Levitiko 16:3-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Aroni azilowa pa bwalo la malo opatulika nazozo: ng'ombe yamphongo ikhale ya nsembe yaucimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale ya nsembe yopsereza.

4. Abvale maraya a m'kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zobvala za kumiyendo pathupi pace, nadzimangire m'cuuno ndi mpango wabafuta, nabvale nduwira yabafuta; izi ndi zobvala zopatulika; potero asambe thupi lace ndi madzi, ndi kubvala izi.

5. Ndipo ku khama la ana a Israyeli atenge atonde awiri akhale a nsembe yaucimo, ndi nkhosa yamphongo imodzi ikhale ya nsembe yopsereza.

6. Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yaucimo, ndiyo yace yace, nacite codzitetezera iye yekha, ndi mbumba yace.

7. Ndipo atenge mbuzi ziwirizo naziimike pamaso pa Yehova pakhomo pa cihema cokomanako.

Levitiko 16