5. ndipo wansembe auze kuti aphe mbalame imodzi m'mbale yadothi pamwamba pa madzi oyenda;
6. natenge nbalame yamoyo, ndi mtengo wankungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, nazibviike pamodzi ndi mbalame yamoyo m'mwazi wa mbalame adaipha pamwamba pa madzi oyenda;
7. nawaze kasanu ndi kawiri iye amene akuti amyeretse khate lace, namuche woyera, nataye mbalame yamoyo padambo poyera.
8. Ndipo iye wakutiayeretsedwe atsuke zobvala zace, namete tsitsi lace lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kucigono, koma agone pa bwalo la hema wace masiku asanu ndi awiri.