Levitiko 13:16-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Kapena mnofu wofiira ukasandukanso, nusandulika wotuwa, afike kwa wansembe,

17. ndi wansembe amuone, ndipo taonani, ngati nthenda yasandulika yotuwa, wansembe amuche woyera wanthendayo; ndiye woyera.

18. Ndipo pamene thupi liri ndi cironda pakhungu pace, ndipo capola,

19. ndipo padali cironda pali cotupa coyera, kapena cikanga cotuuluka, pamenepo acionetse kwa wansembe; ndipo wansembe aone,

20. ndipo taonani, ngati cioneka cakumba kubzola khungu, ndipo tsitsi lace lisanduka lotuwa, pamenepo wansembe amuche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate yabuka m'cirondamo.

21. Koma wansembe akaciona, ndipo taonani, palibe tsitsi loyera pamenepo, ndipo sicinakumba kubzola khungu, koma cazimba, pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri;

22. ndipo ngati capitirira khungu, wansembe amuche wodetsedwa; ndilo khate.

23. Koma ngati cikanga caima pomwepo, cosakula, ndico cipsera ca cironda; ndipo wansembe amuche woyera.

Levitiko 13