Levitiko 11:41-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. Ndipozokwawazonsezakukwawa pa dziko lapansi zikhale zonyansa; musamazidya.

42. Zonse zoyenda cafufumimba, ndi zonse za miyendo inai, kapena zonse zokhala nayo miyendo yambiri ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, musamazidya; popeza ndizo zonyansa.

43. Musamadzinyansitsa ndi cokwawa ciri conse cakukwawa, musamadzidetsa nazo, kuti mukadziipse nazo.

44. Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu; potero dzipatuleni, ndipo muzikhala oyera; pakuti Ine ndine woyera; ndipo musamadziipsa ndi cokwawa ciri conse cakukwawa pansi.

45. Pakuti Ine ndine Yehova amene ndinakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto, ndikhale Mulungu wanu; cifukwa cace mukhale oyera, popeza ine ndine woyera.

46. Ici ndi cilamulo ca nyama, ndi ca mbalame, ndi ca zamoyo zonse zakuyenda m'madzi, ndi ca zamoyo zonse zakukwawa pansi;

Levitiko 11