25. ndipo ali yense akanyamulako nyama ya mtembo wace azitsuka zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
26. Nyama iri yonse yakugawanika ciboda, koma yosagawanikitsa, ndi yosabzikula, muiyese yodetsa; ali yense wakuikhudza adzakhala wodetsedwa.
27. Ndipo iri yonse iyenda yopanda ciboda mwa zamoyo zonse za miyendo inai, muiyese yodetsedwa; ali yense wokhudza mtembo wace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
28. Ndipo iye amene akanyamula mtembo wace atsuke zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; muziyese izi zodetsa.
29. Ndipo izi ndi zimene muziziyesa zodetsedwa mwa zinthu zokwawa zakukwawa pansi; likongwe, ndi mbewa, ndi msambulu mwa mtundu wace;