Levitiko 10:6-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Mose anati kwa Aroni, ndi kwa Eleazara ndi ltamara ana ace, Musawinda tsitsi, musang'amba zobvala zanu; kuti mungafe, ndi kuti angakwiye iye ndi khamu lonse; koma abale anu, mbumba yonse ya Israyeli, alire cifukwa ca motowu Yehova anauyatsa.

7. Ndipo musaturuka pakhomo pa cihema cokomanako, kuti mungafe, pakuti mafuta odzoza a Yehova ali pa inu. Ndipo anacita monga mwa mau a Mose.

8. Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, nati,

9. Usamamwa vinyo, kapena coledzeretsa, iwe ndi ana ako omwe, m'mene mulowa m'cihema cokomanako, kuti mungafe; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu;

Levitiko 10