4. Efraimu iwe, ndidzakucitira ciani? Yuda iwe, ndikucitire ciani? pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam'mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa.
5. Cifukwa cace ndawalikha mwa aneneri; ndawapha ndi mau a pakamwa panga; ndi maweruzo anga aturuka ngati kuunika.
6. Pakuti ndikondwera naco cifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu koposa nsembe zopsereza.
7. Koma iwo analakwira cipangano ngati Adamu, m'mene anandicitira monyenga.
8. Gileadi ndiwo mudzi wa ocita zoipa, wa mapazi a mwazi.
9. Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha pa njira ya ku Sekemu; indedi acita coipitsitsa.