Hoseya 5:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Adzamuka ndi zoweta zao zazing'ono ndi zazikuru kufunafuna Yehova: koma sadzampeza; Iye wadzibweza kuwacokera.

7. Anacita mosakhulupirika pa Yehova, pakuti anabala ana acilendo; mwezi wokhala udzawatha tsopano, pamodzi ndi maiko ao.

8. Ombani mphalasa m'Gibeya, ndi lipenga m'Rama; pfuulani ku Betaveni; pambuyo pako, Benjamini.

9. Efraimu adzasanduka bwinja tsiku lakudzudzula; mwa mapfuko a Israyeli ndadziwitsa codzacitikadi.

10. Akalonga a Yuda akunga anthu osuntha malire; ndidzawatsanulira mkwiyo wanga ngati madzi.

Hoseya 5