Hoseya 4:7-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Monga anacuruka, momwemo anandicimwira; ndidzasanduliza ulemerero wao ukhale manyazi.

8. Adyerera cimo la anthu anga, nakhumbira cosalungama cao, yense ndi mtima wace.

9. Ndipo kudzakhala monga anthu, momwemo wansembe; ndipo ndidzawalanga cifukwa canjira zao, ndi kuwabwezera macitidwe ao.

10. Ndipo adzadya, koma osakhuta; adzacita cigololo, koma osacuruka; pakuti waleka kusamalira Yehova.

11. Cigololo, ndi vinyo, ndi vinyo watsopano, zicotsa mtima,

12. Anthu anga afunsira ku mtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wacigololo wawalakwitsa, ndipo acita cigololo kucokera Mulungu wao.

13. Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi miniali, ndi mkundi; popeza mthunzi wace ndi wabwino, cifukwa cace ana anu akazi acita citole, ndi apongozi anu acita cigololo.

Hoseya 4