Hoseya 4:16-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Pakuti Israyeli wacita kuuma khosi ngati ng'ombe yaikazi yaing'ono youma khosi; tsopano Yehova adzawadyetsa ngati mwana wa nkhosa ku thengo lalikuru.

17. Efraimu waphatikana ndi mafano, mlekeni.

18. Cakumwa cao casasa, acita citole kosalekeza; akuru ao akonda manyazi kwambiri.

19. Mphepo yamkulunga m'mapiko ace, ndipo adzacita manyazi cifukwa ca nsembe zao.

Hoseya 4