14. Sindidzalanga ana anu akazi pocita citole iwo, kapena apongozi anu pocita cigololo iwo; pakuti iwo okha apambukira padera ndi akazi acitole, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa kucitole; ndi anthu osazindikirawo adzagwetsedwa camutu.
15. Cinkana iwe, Israyeli, ucita citole, koma asaparamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.
16. Pakuti Israyeli wacita kuuma khosi ngati ng'ombe yaikazi yaing'ono youma khosi; tsopano Yehova adzawadyetsa ngati mwana wa nkhosa ku thengo lalikuru.
17. Efraimu waphatikana ndi mafano, mlekeni.